
Rhapsody Global Club ( Mandate 1B ROR Influences )
February 28, 2025 at 09:34 PM
Rhapsody Chichewa
Sat, Mar 1, 2025
WANGWIRO NDI WATHUNTHU
koma chipiliro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale atunthu (amphumphu) ndi opanda chilema, osasowa kanthu konse (Yakobo 1:4).
Pali Mau awiri ofunika amene ndikufuna muwaonetsetse m’ndime tangowerengayi; mau oti "ungwiro" ndi "utunthu." Mau akuti "utunthu" amachokera ku mau a chigiliki oti “teleios,” amene amatanthauza kukwanira. Pamene mau oti "ungwiro," anatanthauzilidwa kuchokera ku mau a chigiliki oti “holoklēros” ndipo amatanthauza kukhala ndi ziwalo zonse zokwanira; kudzadza, kulungama, palibe chofunikira chomwe chikusowapo. Ichi ndiye chifuniro cha Mulungu pa inu.
Pa Akolose 4:12, Mzimu, kudzera mwa mtumwi Paulo, amatiuza chinthu chokhudza kwambiri. Akuti, “akupatsani moni Epafra ndiye wa kwa inu, ndiye kapolo wa Khristu Yesu, wakulimbira chifukwa cha inu m’mapemphero ake masiku onse, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m’chifuniro chonse cha Mulungu.” Apanso mau oti, “amphumphu” ndi ochoka ku mau a chigiliki oti “teleios.” Kenaka Paulo akutipatsanso mau ena, “plēroō” (achigiliki), amene atanthauzilidwa kuti "okwanira."
“Plēroō” amatanthauza kudzadza mbuu, kufika pamwamba pafupi kusefukira. Zimaonetseranso kukhutitsidwa, kukwaniritsa cholinga, kapena kufikitsa chinthu kumapeto. Izi zimabweretsa funso lofunika; lakuti kodi mkatimo muli chani chomwe chikudzadza mpaka pamwamba kapena kutsala pangono kusefukira? Zimatikumbutsa pemphero la Paulo la Mzimu ku Akolose 1:9, lakuti Akhristu aku Akolosi adzazidwe, akhathamire ndi chidziwitso cha chifuniro cha Mulungu mu nzeru zonse ndi kumvetsetsa kwa uzimu: “mwa ichi ifenso, kuyambira tsiku limene tinamwa, sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziwitso cha Mzimu.”
Pa ndime yotsatilaro la 10 amatiuza cholinga cha chidzalo cha chifuniro chakechi mu nzeru ndi kumvetsetsa kwa uzimu: “kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m’chizindikiritso cha Mulungu” (Akolose 1:10). Taganizirani izi! Mulungu akufuna mukhale angwiro ndi anthunthu; okwaniritsidwa, amphumphu, odzazidwa ndi chidziwitso cha chifuniro chake kuti mukhale moyo oyenera Iye, kumusangalatsa mu zonse, kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, pemene mukuchulukira muchidziwitso cha Mulungu. Aleluya!
PEMPHERO
Wokondedwa Atate, zikomo chifukwa cha Mau anu amene amandisintha ndipo amandilunjikitsa ndi chifuniro chanu chagwiro. Pemene ndikulingalira pa choonadi chanu, ndimayima wangwiro ndi wanthunthu mu zonse zomwe mwakonzera moyo wanga, otsogozedwa ndi Mzimu wanu mu chidzalo ndi umphumphu; sindisowa kanthu ndipo ndimabweretsa ulemelero ku Dzina lanu, m’Dzina la Yesu. Amen.
WERENGANINSO:
2 Timoteo 3:16-17; Aefeso 3:19; Aefeso 4:13
NDONDOMEKO YOWERENGA BAIBULO CHAKA CHIMODZI
Marko 9:14-32 & Numeri 7-8
NDONDOMEKO YOWERENGA BAIBULO ZAKA ZIWIRI
Mateyu 19:1-12 & Eksodo 10
WhatsApp Chanel for rhapsody Translation :
https://whatsapp.com/channel/0029Va9SJ9OHFxP0Xh4KCN3F