
Rhapsody Global Club ( Mandate 1B ROR Influences )
June 12, 2025 at 05:25 PM
Rhapsody Chichewa
Fri Jun 13 2025
KHALANIBE OLIMBA—KANANI KUKHAZIKIKA PA ZOSAYENELA
Pamene ukuwoloka nyanja,ndidzakhala nawe; ndipo pamene ukuwoloka mitsinje, sidzakukokolola .Pamene ukudutsa pa moto, sudzapsa; lawi la moto silidzakutentha (Yesaya 43:2).
Mutha kupezeka mu nyengo yakuti mukukanthidwa ndi zipsyinjo komanso mazunzo kumbali zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino; musataye mtima. Zomwe mukuchita zili ndi tsogolo. Ntchito zanu mwa Ambuye sizachabe; ndiza cholinga ndipo ndizamuyaya. Mulungu sanalonjeze kuti zonse zikhala bwino kapena popanda zovuta. Anatiuza kuti padzakhala zovuta, mayesero, ndi adani. Koma pakati pa zonsezi, Iye anatitsimikizira za kupezeka kwake ndi chigonjetso.
Kumbukirani zimene tawerenga m’ndime yathu yotsogolera; Iye sananene kuti sipadzakhala namondwe kapena moto. Lonjezolo silokhudza kusapezeka kwa zovuta koma ndi chitsimikizo cha kupezeka Kwake ndi chitetezo kwa inu pakati pa masautso. Zimakuthandizani kumvetsetsa chifukwa chomwe amanenera kuti, “Abale, muchiyese ngati chimwemwe chenicheni nthawi zonse pamene mukukumana ndi mayesero amitundumitundu” (Yakobo 1:2).
Baibulo pa Danieli chaputala 3 limatiuza za Sadirake, Mesake, ndi Abedinego, anyamata atatu amene anakhalabe olimba m’chikhulupiriro chawo ngakhale ankatsutsidwa kwambiri. Nthawi zambiri, nkhani yawo imakumbukiridwa chifukwa cha ng'anjo yamoto ndi kupulumutsidwa kwawo mozizwitsa, koma pali zambiri. Asanaponyedwe m’motomo, anatsutsidwa, kukanidwa ndi kuneneredwa zabodza. Anapirira kudedwa ndi kutsutsidwa chifukwa chakuti anakana kusunthika pa chikhulupiriro chawo.
Malemba pa 2 Akorinto 4:17 amati, "Pakuti masautso athu ndi opepuka ndi a kanthawi, koma akutitengera ulemerero wamuyaya umene ndi wopambana kwambiri." Choncho, pali zinthu zomwe muyenera kukumana nazo, kudutsamo, kuyima motsutsana nazo kuti mukhale moyo waumulungu womwe Yehova wakupatsani. Pakhoza kukhala adani kumbali zonse, koma ngakhale pakati pa zonsezo, ndinu woposa mgonjetsi. Malemba pa 2 Timoteyo 3:12 amati, “Kunena zoona, munthu aliyense amene akufuna kukhala moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi.”
Iye amene ali mwa inu ndi wamkulu kuposa amene ali m’dziko lapansi (1 Yohane 4:4). Iye akutitsimikizira pa Mateyu 28:20 kuti, "Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano." Khazikitsani maso anu pa zam'tsogolo ndi pa ulemerero Wake. Kanani kusokonezedwa ndi zovuta zosakhalitsa. Khalani ndi chidaliro kuti zingavute bwanji, Mawu ake adzapambana m’moyo wanu, ndipo ulemerero wake udzavumbulutsidwa mwa inu komanso kudzera mwa inu nthawi zonse.
Prayer / Confession
Ndaima nji mchikhulupiriro, mosatengela zopinga kapena zotsutsa, chifukwa Wamkuluyo amakhala mwa ine. Mawu anu amandiyika ine pamwamba pa mayesero aliwonse, ndipo ndimayenda m’chigonjetso chosatha. Zikomo chifukwa cha kupezeka kwanu, chitetezo chanu, ndi Mawu anu omwe salephera, m'Dzina la Yesu. Amen.
Further study
1 Akorinto 15:57-58; Aroma 8:31-37; 2 Akorinto 4:17 AMPC
1-year bible reading plan
Machitidwe 4:1-31 & 2 Mbiri 16-19
2-year bible reading plan
Luka 1:26-38 & Deuteronomo 11
WhatsApp Chanel for rhapsody Translation :
https://whatsapp.com/channel/0029Va9SJ9OHFxP0Xh4KCN3F
🙏
1