Rhapsody Global Club ( Mandate 1B ROR Influences )
Rhapsody Global Club ( Mandate 1B ROR Influences )
June 13, 2025 at 07:03 PM
Rhapsody Chichewa Sat Jun 14 2025 MPHAMVU YA MASOMPHENYA NDI KULINGALIRA Tsono Yakobo anatenga nthambi zaziwisi za mitengo ya mkundi, alimoni ndi puleni nazisenda kuchotsa makungwa ake mpaka mtengo woyera wamʼkati kuonekera (Genesis 30:37). Nkhani ya Yakobo ku Genesis 30 ndi 31 ndi chionetsero chochititsa chidwi cha mphamvu ya masomphenya ndi kulingalira. Pamene Yakobo anavomera kugwira ntchito kwa Labani, analonjezedwa kuti adzapatsidwa ng’ombe monga malipiro. Komabe, Labani anasintha mobwerezabwereza mawuwo n’kumunyenga Yakobo. Koma Yakobo, kudzera mu nzeru yaumulungu ndi luso la kulenga, anatembenuza zinthu. Yakobo anatenga thambi zaziwisi za mtengo wa mkundi, ndi za alimoni, ndi za mtengo wa puleni, nazisenda kuchotsa makungwa ake mpaka mtengo woyera wamʼkati kuonekera. Atatero anayika nthambi zija mʼmagome omwe nyamazo zimamwera madzi. Nyama zikamakwerana patsogolo pa nthambizo, zinkabala ana amene Yakobo ankafuna. Pambuyo pake, Yakobo sanafunenso ndodozo. ndipo analekanitsa ana a ziweto amene anali ndi zamawanga-mawanga, ndi zamathothomathotho, naziika pamaso pa ng'ombe zamphamvu. Pochita zimenezi, anazipatsa nkhosazo masomphenya, ndipo zinkabereka mogwirizana ndi zimene zinkaona. Njira imene anagwiritsa ntchito Yakobo inali chiwonetsero champhamvu cha kulenga kumene kumachitika ndi masomphenya. Anagwiritsa ntchito luso lake la kulingalira kuti asinthe zotsatira zake. Pamene ng’ombe zamphamvuzo zinatenga bere, Yakobo anayika ndodozo pamaso pawo, kuonetsetsa kuti zabala ana amphamvu, osiririka. Pamene ng’ombe zinali zofooka, sankagwiritsa ntchito ndodozo, choncho zofooka zinali za Labani. M’kupita kwa nthawi, ziweto za Yakobo zinakula ndi kuchuluka, pamene za Labani zinali zofooka. Kupambana kwa Yakobo kunali mwa vumbulutso laumulungu. M’maloto anaona nkhosa zamphongo zikudumphira ng’ombe ngati za amichocholozi, zamawanga mawanga, ndi zamathothomathotho. Mngelo anatsimikizira masomphenyawo, nati, “Tayangʼana ndipo taona kuti atonde onse okwerana ndi ziweto ali amichocholozi, amawangamawanga kapena a mathothomathotho....” (Genesis 31:12). Izi nzofunika kwambiri! Muli ndi kuthekera kolenga tsogolo lomwe mukufuna poyang'ana zomwe mukufuna kuwona. Pangani masomphenya omwe mukufuna ndi malingaliro anu. Kudzera m’Mau ndi mphamvu ya Mzimu Woyera akugwira ntchito mwa inu, mukhoza kudzilengela kapena kudziumbira zinthu zooneka ndi zogwirika. Aleluya! Prayer / Confession Wokondedwa Atate, zikomo pondipatsa kuthekera kowona ndi kulenga tsogolo langa lofunidwa kudzera mu mphamvu ya masomphenya ndi Mawu anu. Pamene ndigwiritsa ntchito luso langa la kulingalira, motsogozedwa ndi Mzimu wanu, ndimamanga moyo wanga mogwirizana ndi cholinga chanu cha umulungu, ndi kupambana ndi kukula m'madera onse. Ndili ndi mphamvu zokhudza dziko langa ndikukwaniritsa logolo langa, m'dzina la Yesu. Amen. Further study Genesis 13:14-17; Habakuku 2:2; Aefeso 3:20 1-year bible reading plan Machitidwe 4:32-5:1-11 & 2 Mbiri 20-22 2-year bible reading plan Luka 1:39-56 & Deuteronomo 12 WhatsApp Chanel for rhapsody Translation : https://whatsapp.com/channel/0029Va9SJ9OHFxP0Xh4KCN3F
🙏 1

Comments