Department of Climate Change and Meteorological Services
                                
                            
                            
                    
                                
                                
                                February 3, 2025 at 11:22 AM
                               
                            
                        
                            3 February, 2025
CHIDZIWITSO CHOKHUDZA NAMONDWE FAIDA 
Tsiku ndi nthawi yosindikizira: Lolemba pa 3 February, 2025; 12:00pm. 
Kusindikiza kwa nambala : TC2024/25-19 
🌀🌀
Nthambi Yoona za Nyengo ndi Kusintha kwa Nyengo ikudziwitsa mtundu wa a Malawi kuti NAMONDWE wotchedwa FAIDA wabadwa m’nyanja ya m’chere ya India kumpoto chakumvuma kwa dziko la Madagascar. Namondweyu ali pa mlingo wa 998hPa ndipo akuyenda ndi liwiro la 19km/hr kumalowera kum’mpoto chakuzambwe molunjika ku gombe la dziko la Madagascar. 
Pakadali pano, Namondwe Faida sakukhudza nyengo ya ku Malawi kuno. 
Ngakhale izi zili chonchi, Ulosi wa momwe NAMONDWE FAIDA atayendere ukusonyeza kuti namondweyu akhodza kufika mu Mozambique Channel (dera lapakati pa Mozambique ndi Madagascar) mwinanso mkufika oyandikila ndi dziko lathu lino. 
Nthambi yoona zanyengo ikhala ikupitilira kuunikila namondweyu ndi kudziwitsa mtundu wa a Malawi.  
FacebooK: https://web.facebook.com/MetMalawiDCCMS
                        
                    
                    
                    
                    
                    
                                    
                                        
                                            👍
                                        
                                    
                                        
                                            ❤️
                                        
                                    
                                        
                                            😢
                                        
                                    
                                        
                                            😮
                                        
                                    
                                        
                                            🙏
                                        
                                    
                                    
                                        6