Department of Climate Change and Meteorological Services WhatsApp Channel

Department of Climate Change and Meteorological Services

11.8K subscribers

About Department of Climate Change and Meteorological Services

Welcome to the Department of Climate Change and Meteorological Services channel. Stay updated on #malawi weather, climate, alerts and news.

Similar Channels

Swipe to see more

Posts

Department of Climate Change and Meteorological Services
Department of Climate Change and Meteorological Services
5/15/2025, 2:52:48 PM

#ZBSNews Anthu atatu akuti akusowa bwato lomwe anakwera litagudubuzika pa nyanja ya Chilwa dzulo masana. Malinga ndi zomwe tapeza bwatolo lomwe linali ndi anthu 8 komanso matumba a mpunga oposa 80 akuti lagudubuzika pafupi ndi doko la Lungazi m'boma la Zomba. M'neneri wa Polisi mchigawo chaku m'mawa a Patrick Mussa, apempha nthawi asanayankhulepo pa nkhaniyi. (by Raphael Mlozoa-Zomba:05/15/2025) #malawismostfollowedpage

😢 ❤️ 😮 🙏 29
Department of Climate Change and Meteorological Services
Department of Climate Change and Meteorological Services
5/15/2025, 11:14:19 AM

NYENGO YA USIKU UNO NDI MAWA PA 16 MAY 2025 🌤🌧🌊 Tiyembekezere nyengo yozizira m’madera ambiri koma mvula igwa m’madera ochepa makamaka am’chigawo cha kumpoto usiku uno ndi mawa m’mawa. Mawa masana, kudzakhala kwa nyengo ya mitambo yapatalipatali ndipo kudzafunda koma mvula idzagwa m’madera ochepa. 🌬🌊LANGIZO: Pomwe Mphepo ya Mwera ikuchepa mphamvu, anthu omwe amagwiritsa ntchito nyanja zathu monga asodzi, akulimbikitsidwa kukhalabe osamala mpaka panyanja patakhala pa bata. Mphepo: Iziomba mochokera kum’mwera cha kumvuma... Loweruka: Kudzakhala kwa mitambo komanso kudzafunda... Facebook: https://web.facebook.com/MetMalawiDCCMS Website: https://www.metmalawi.gov.mw/products/daily-forecast/weather-forecast-16-may-2025/

Post image
👍 ❤️ 6
Image
Department of Climate Change and Meteorological Services
Department of Climate Change and Meteorological Services
5/16/2025, 2:13:22 PM

WEATHER FORECAST FOR TONIGHT AND TOMORROW 17TH MAY 2025 ⛅🌧️ Expect cold weather over most areas while with fog patches and isolated rain over northern areas tonight and tomorrow morning. Partly cloudy and warm conditions over most areas while with isolated rain over few highlands and northern lakeshore areas tomorrow afternoon. ADVISORY: Avoid using a charcoal burner in a poorly ventilated room, as it may cause suffocation and result in death WINDS: Generally southeasterly… FORECAST FOR SUNDAY: Partly cloudy and warm conditions… Facebook: https://web.facebook.com/MetMalawiDCCMS Website: https://www.metmalawi.gov.mw/products/daily-forecast/weather-forecast-17-may-2025/

Post image
Image
Department of Climate Change and Meteorological Services
Department of Climate Change and Meteorological Services
5/16/2025, 7:36:53 AM

16 May 2025 Ku Njuli ku Chiradzulu kwacha kwa dzuwa 🌞🌞🌞🌞. Photo Credit: Nasuluma

Post image
❤️ 👍 😂 😢 🙏 13
Image
Department of Climate Change and Meteorological Services
Department of Climate Change and Meteorological Services
5/14/2025, 1:25:37 PM

NYENGO YA USIKU UNO NDI MAWA PA 14 MAY 2025 🌧 Tiyembekezere nyengo ya Chiperoni yomwe ndi nyengo ya mvula, ya mphepo, ya mitambo yambiri ndi yozizira komanso ya chifunga kudzayamba kuchepa mphamvu mawa lino pa 15 May 2025. 🌊⚠️CHENJEZO: Mphepo ya Mwera ya liwiro loposa 50km/h ikuyembekezeka kupitilira kuomba pa nyanja zathu monga nyanja ya Malawi ndi nyanja zina. Mphepoyi ikuyekezeka kuyamba kuchepa mphamvu kuyambira mawa lino pa 15 May 2025. Ngakhale zili choncho, tikulimbikitsabe onse omwe amagwiritsa ntchito nyanjazi kuti akapitilize kukhala osamala. MPHEPO: Iziomba kuchokera kum’mwera cha kumvuma... Facebook: https://web.facebook.com/MetMalawiDCCMS Website: https://www.metmalawi.gov.mw/products/daily-forecast/weather-forecast-15-may-2025/

Post image
❤️ 3
Image
Department of Climate Change and Meteorological Services
Department of Climate Change and Meteorological Services
5/16/2025, 2:09:45 PM

NYENGO YA USIKU UNO NDI MAWA PA 17 MAY 2025 🌤🌧 Tiyembekezere nyengo yozizira m’madera ambiri koma kukhala kwa chifunga komanso kugwa mvula m’madera ochepa am’chigawo cha kumpoto usiku uno ndi mawa m’mawa. Mawa masana, kudzakhala kwa nyengo ya mitambo yapatalipatali ndipo kudzafunda koma mvula idzagwa m’madera ochepa makamaka m’madera okwera ndi am’mphepete mwa nyanja ya Malawi ku chigawo chakumpoto. LANGIZO: Tisagone ndi mbaula yoyaka mnyumba kuopa kufera kutulo. MPHEPO: Iziomba mochokera kum’mwera cha kumvuma... LAMULUNGU: Kudzakhala kwa mitambo yapatalipatali komanso kudzafunda... Facebook: https://web.facebook.com/MetMalawiDCCMS Website: https://www.metmalawi.gov.mw/products/daily-forecast/weather-forecast-17-may-2025/

Post image
🙏 1
Image
Department of Climate Change and Meteorological Services
Department of Climate Change and Meteorological Services
5/17/2025, 9:48:32 AM

17 May 2025 Dowa Madisi kwacha kwa ka Dzuwa☀️🌤☀️☀️ ndithu. Enjoy your weekend Photo Credit: (Malawi Weather Chasers) Facebook: https://web.facebook.com/MetMalawiDCCMS

Post image
❤️ 👍 😮 6
Image
Department of Climate Change and Meteorological Services
Department of Climate Change and Meteorological Services
5/16/2025, 2:23:22 PM

16 May 2025 English: Avoid using a charcoal burner in a poorly ventilated room, as it may cause suffocation and result in death. Chichewa: Tisagone ndi mbaula yoyaka mnyumba kuopa kufera kutulo. Tumbuka: Tileke kugona na mbaula yakugolera munyumba kopa kuti tingafwira kutulo. Yao: Tuligose pagona ni mbaula jana moto pakogopela kuwila kulugono. Tonga: Tileki kugona ndi mbaula yakubuka munyumba kopa kufwiya kutulu. Facebook: https://web.facebook.com/MetMalawiDCCMS

Post image
😂 👍 🙏 ❤️ 18
Image
Department of Climate Change and Meteorological Services
Department of Climate Change and Meteorological Services
5/15/2025, 7:18:25 AM

15 May 2025 🌦🌤⛅️🌤 Nyengo ya Chiperoni ndiye yachepa mphamvu Kum'mwera ndi pakati , zikatero Mphepo ya Mwera pa nyanja ichepanso mphamvu. Koma nyengo ya Mvula ipitirira m'madera ena am'chigawo cha kumpoto. Facebook: https://web.facebook.com/MetMalawiDCCMS Photo Credit: Malawi Weather Chasers (Place: Mponela, Dowa)

Post image
👍 ❤️ 😂 🙏 13
Image
Department of Climate Change and Meteorological Services
Department of Climate Change and Meteorological Services
5/14/2025, 7:54:33 AM

Mphepo ya Chiperoni yomwe ikuomba mdziko muno itionetsa zinthu. Mwachitsanzo anthu ambiri m'township ya Limbe, anavala mawovololo akuchipatala otchedwa kuti coverall interfaces. Awa ndi ma ovololo omwe ankapezeka kwambiri ndi anthu za achipatala munyengo ya muliri wa Covid 19. Pano zovalazi zikugulitsidwa pa mitengo ya K 3,500- kulekeza K4,000. Padakali pano, nthambi ya nyengo yati mphepoyi ichepa mphamvu lachinayi lino. #mijnews #malawinews #malawi -Nicolas Mbonela-

Post image
😂 👍 😢 ❤️ 🙏 46
Image
Link copied to clipboard!