
Department of Climate Change and Meteorological Services
February 4, 2025 at 03:24 AM
Mtsinje wa Limbe wasefukira
Mvula yamphamvu yomwe yagwa mu mzinda wa Blantyre Lolemba masana, yachititsa kuti mtsinje wa Limbe usefukire ndikukhudza nyumba zochuluka monga m'madera a Chiwembe, Che Mmadi ndi ena.
MBC yapeza kuti nyumba zina zagwa pomwe zina zachita ming'alu kutsatira madzi osefukirawa kuphatikizapo zina zomwe anazimanga pafupi ndi mtsinjewu.
Mvulayi yomwe inagwa pafupifupi maola atatu, inachititsanso kuti galimoto zirephere kudutsa pa mlatho odutsa kuchoka ku Limbe mbali ya polisi ndikupita kumsika pomwe mtsinjewu unasefukira.
Galimoto zimalepheranso kuoloka kuchokera pa Hardware ndikufika pa Yiannakis ku Limbe pomwenso madzi anadzadza ndipo galimoto zina zinazima kaamba kakuchuluka kwa mvulayi.
Nakonso ku msika, m'mbali mwa mtsinje omwewu, minibus ina inamira kupitilira theka, madzi a mtsinje wa Limbe atayamba kusefukira.
Pakadali pano, anthu omwe alankhula ndi MBC ati aka ndikoyamba kuona mtsinjewu utasefukira motero, pomwe malipoti akuti mvula ikugwabe ku Limbe usiku uno.
Olemba Blessings Kanache
#mbcdigital
#manthu
😢
👍
😮
23