Department of Climate Change and Meteorological Services
Department of Climate Change and Meteorological Services
February 14, 2025 at 07:20 AM
14 February, 2025 09:00 AM ⛈️⛈️⛈️ ⛈️ Mvula ⚡Mphenzi Chithunzi chaposachedwapa cha makina amakono ( satellite imagery) chikuwonetsa mabingu (omwe akuonekera mu makaka oyera) ayamba kubadwa m'madera ena m’dziko muno monga ku Chiradzulu, Zomba, Blantyre, Mangochi, Dedza, Nkhotakota, Ntchisi. Mabinguwa akuyembekezeka kufalikira m'madera ena kuphatikizapo madera ena am'chigawo chapakati . Pali chiyembekezo chachikulu chakuti kumasanaku agwetsa mvula yomwe ingabwere ndi mphenzi. Tikhale tcheru chifukwa nyengo itha kusintha nthawi ina iliyonse. CHINA MWA ZIOPSEZO 1. Mphenzi MALANGIZO 1. Mvula ya mabingu ikamagwa osabisala pansi pa mitengo 2. Tibisale m'nyumba kukamagwa mvula ya mabingu. #khalaniozindikiradziwanizanyengo
👍 😮 🙏 7

Comments