Department of Climate Change and Meteorological Services
Department of Climate Change and Meteorological Services
February 15, 2025 at 10:34 AM
Mvula ya mphamvu yawononga katundu osiyanasiyana komanso kugwetsa nyumba m'midzi ya Khumbulani ndi Nadiwa kwa mfumu yaikulu Katunga m'boma la Chikwawa. Khansala wa dera la Mwamphanzi, Wyson Bush wati anthu ambiri akusowa pokhala kaamba koti nyumba zawo zawonongeka. Iye watinso madzi ochuluka anatseka msewu wa Thabwa-Blantyre koma pakadali pano aphwera ndipo galimoto zayambanso kudutsa. Bush watinso pa Domasi pomwe madzi anadula msewu wa M1pakupereka chiwopsyezo maka kwa oyenda pansi chifukwa padzaza madzi ndi matope. Iye wawonjezera kuti ku dera la Mfera, mtsinje wa Nakatale wasefukira kwambiri ndipo madzi alowa m'nyumba za anthu. #malawinews #malawi #mijnews -Emmanuel Malunga-
😢 👍 🙏 15

Comments