Department of Climate Change and Meteorological Services
Department of Climate Change and Meteorological Services
February 19, 2025 at 07:17 AM
19 February 2025 09:00 AM ⛈️⛈️⛈️ ⛈️ Mvula ⚡Mphenzi 🌊🚣‍♀️ Madzi osefukira mwadzidzidzi Chithunzi chaposachedwapa cha makina amakono ( satellite imagery) chikuwonetsa mabingu omwe ayamba kubadwa m'madera ena am'zigawo za kum'mwera ndi kumpoto monga ku Chikwawa komanso ku Rumphi. Mabinguwa akuyembekezeka kufalikira m'madera enanso ochuluka m'maola angapo akudzawa monga ku Phalombe, Nsanje, Blantyre, Thyolo, Lilongwe, Mchinji, Dowa, Mzimba, Mulanje mongotchulapo madera ochepa, zomwe zikupereka chiyembekezo cha mvula m'madera amenewa ndi enanso ozungulira. Tikhale tcheru chifukwa nyengo itha kusintha nthawi ina iliyonse. ZINA MWA ZIOPSEZO 1. Mphenzi 2. Madzi osefukira mwadzidzidzi MALANGIZO 1. Mvula ya mabingu ikamagwa osabisala pansi pa mitengo. 2. Tibisale m'nyumba zolimba bwino kukamagwa mvula ya mabingu. 3. Osaoloka madzi osefukira kapena omwe akuthamanga kwambiri. #khalaniozindikiradziwanizanyengo
👍 🙏 ❤️ 😢 10

Comments