Department of Climate Change and Meteorological Services
Department of Climate Change and Meteorological Services
February 19, 2025 at 03:06 PM
19 February 2025 17:00 PM (Uthenga wachiwiri) ⛈️⛈️⛈️ ⛈️ Mvula ⚡Mphenzi 🌊🚣‍♀️ Madzi osefukira mwadzidzidzi Chithunzi chaposachedwapa cha makina amakono ( satellite imagery) chikuwonetsa mabingu (omwe akuonekera mu mtundu wachikasu) akukhudza madera ena m’dziko muno monga Lilongwe , Chiradzulu, Phalombe, Dowa, Dedza. Mabinguwa ali m'magawo osiyanasiyana: ena angoyamba kumene, ena akugwetsa mvula, ndipo enanso akuzilala. Pali chiyembekezo chachikulu kuti usiku uno apitiriza kugwetsa mvula m'madera ena monga am'mphepete mwa nyanja yathu ya Malawi. Tikhale tcheru chifukwa nyengo itha kusintha nthawi ina iliyonse. ZINA MWA ZIOPSEZO 1. Mphenzi 2. Madzi osefukira mwadzidzidzi MALANGIZO 1. Mvula ya mabingu ikamagwa osabisala pansi pa mitengo 2. Tibisale m'nyumba zolimba bwino kukamagwa mvula ya mabingu 3. Tisaoloke madzi omwe asefukira kapena omwe akuthamanga kwambiri. #khalaniozindikiradziwanizanyengo
👍 🙏 ❤️ 10

Comments