
Department of Climate Change and Meteorological Services
May 15, 2025 at 02:52 PM
#zbsnews
Anthu atatu akuti akusowa bwato lomwe anakwera litagudubuzika pa nyanja ya Chilwa dzulo masana.
Malinga ndi zomwe tapeza bwatolo lomwe linali ndi anthu 8 komanso matumba a mpunga oposa 80 akuti lagudubuzika pafupi ndi doko la Lungazi m'boma la Zomba.
M'neneri wa Polisi mchigawo chaku m'mawa a Patrick Mussa, apempha nthawi asanayankhulepo pa nkhaniyi.
(by Raphael Mlozoa-Zomba:05/15/2025)
#malawismostfollowedpage
😢
❤️
😮
🙏
29