Department of Climate Change and Meteorological Services
Department of Climate Change and Meteorological Services
May 19, 2025 at 02:11 PM
NYENGO MSABATA IKUBWERAYI KUYAMBIRA PA 19 MAY MPAKA PA 25 MAY 2025 🌤🌦Nyengo ya dzuwa mwapatalipatali komanso yozizira ipitirira m’madera ambiri. Koma nyengo ya mvula ikuyembekezeka m’madera ochepa makamaka am’chigawo cha kumpoto mpaka Lachitatu lino pa 21May 2025. 🌧🌨💨Koma kuyambira Lachinayi pa 22 May 2025 tiyembekezere nyengo ya Chiperoni yomwe ndi nyengo ya mphepo, ya mitambo, yozizira, ya chifunga komanso ya mvula m’madera ambiri kamba ka mpweya wa chinyontho komanso wozizira wochokera kum’mwera chakumvuma mu nyanja ya m'chere ya India. ⚠️🌊Mphepo ya Mwera idzaombanso mwa mphamvu panyanja ya Malawi ndi nyanja zina. Facebook: https://web.facebook.com/MetMalawiDCCMS
Image from Department of Climate Change and Meteorological Services: NYENGO MSABATA IKUBWERAYI  KUYAMBIRA PA 19 MAY MPAKA PA 25 MAY 2025  �...
👍 ❤️ 🙏 9

Comments