Department of Climate Change and Meteorological Services
Department of Climate Change and Meteorological Services
June 3, 2025 at 12:21 PM
#update Apolisi m’boma la Karonga alimbikitsa asodzi a m’bomali kuti adzitsatira zanyengo asanalowe m’madzi. Pempholi ladza kutsatira imfa ya anthu atatu omwe amira pa nyanja ya Malawi m’masiku anayi okha kuyambira pa May 30 mpaka June 2, 2025. Wofalitsa nkhani za apolisi ku Karonga, a Margret Msiska, ati omwe amwalirawa ndi Lowland Ng’ambi wazaka 29, Jonas Mtawali wazaka 32, komanso munthu wina yemwe sadadziwike. Msiska wati Ng’ambi anasowa pa 1 June, 2025 atapita kukawedza nsomba ndipo thupi lake linapezeka pa 2 June, 2025 likuyandama m’dera la Gumi pamene pa tsiku lomwelo, thupi la munthu wosadziwikayo, lomwe linali litayamba kuwola, linaonekanso likuyandama pafupi ndi malo owedzera a Israel m’mudzi mwa Mwandovi . Thupi la Mtawali amene anamira pa 30 May, 2025 bwato lake litatembunuka/ Kugudubuka chifukwa cha mafunde, linaoneka pa June 2. Wolemba Blessingz Mtika, Karonga #mbcdigital #manthu
😢 👍 🙏 7

Comments