
Department of Climate Change and Meteorological Services
June 9, 2025 at 08:20 AM
*Mphepo ya Mwera iwomba pa nyanja zathu kuyambira Lachitatu, pa 11 June 2025.*
*Chiopsezo:*
Mphepo ya mphamvu ya Mwera idzachititsa mafunde owopsa pa nyanja ya Malawi ndi pa nyanja zina kuyambira Lachitatu, pa 11 June mpaka Lolemba, pa 16 June 2025.
*Mafundewa akhoza:*
1. kudzachititsa mabwato kapena maboti kudzamira.
2. kudzasokoneza ntchito za panyanja monga usodzi ndi maulendo.
3. kudzachititsa anthu kutaya miyoyo ndi katundu.
*Malangizo:*
1. Pewani maulendo a pa nyanja, makamaka pogwiritsa ntchito maboti ang’onoang’ono, mu nthawiyi.
2. Asodzi akulangizidwa kudzaimitsa usodzi mpaka panyanja padzakhale pa bata.
3. Khalani tcheru ndipo tsatirani mwachidwi mauthenga azanyengo ochokera ku DCCMS.
4. Madongosolo onse ofuna kukasangalala pa nyanja pa nthawiyi ayimitsidwe kaye. .
5. Dziwitsani adindo mwamsanga za ngozi iliyonse.
Zambiri: https://www.metmalawi.gov.mw/weather-warnings/strong-mwera-winds-on-our-lakes-from-thur/
Komanso: https://severeweather.wmo.int/

👍
1