Malawi Job Vacancies and adverts
Malawi Job Vacancies and adverts
June 11, 2025 at 05:40 PM
Pali zinthu zina zofunika kumvesa komanso kukhala ndi chikhulupililo Ambili mukaona kuti wina waimbilidwa phone kuti akayambe ntchito mumabwela ku inbox kumati inenso ndifufuzileni sanandiimbile, keep in mind aliyense ali ndi nthawi yake. Ena amapeza ntchito soon after graduation pamene ena zimatha zakazaka asanapeze ntchito. Pali zinthu zina zomwe tikuenela kusamala tikamapanga apply, utha kumangoti samandiitana ku ma interview vuto uli iwe 1. Updating CV to withstand competition and to match the job description. Ena CV yanu yatha zaka 5 no update, kumangojambula basi kumatumiza not even in PDF form let alone naming it. Vacancy kungoona job title basi mwaponya kale osawelenganso kuti akufuna chani. 2. Come up with a good cover letter. Phuzilani ndithu chizungu choti muzigwilisa ntchito polemba kalata. Kalata yako ndi imene imapeleka chidwi kwa mabwana kuti aonenso CV ndi zina. Koma zongokandakandazi sapitilizanso kuwelenga. 3. Understand kuti akufuna mutumize zinthu ziti. Is it cover letter+CV+ certificates, or cover letter+ CV only, or CV only and send exactly what they want you to send. 4. Read carefully mode of application kuti muzitumiza koyenela. Ambili ma application anu mukumatumiza kolakwika because simuwelenga bwinobwino kaya ndi phuma.
👍 🙏 ❤️ 😢 😂 31

Comments