Capital FM Malawi
Capital FM Malawi
May 27, 2025 at 07:56 AM
#cdedi_presser: Pankhani yakusowa kwa Sugar, Namiwa akuti ndizodabwitsa kuti dziko lino lili pampanipani pamene kampani zopanga Sugar zikupititsa katunduyu kunja kwa dziko lino. Iye akuti nduna yoona zamalonda Vitumbiko Mumba ibwere poyera kufotokozera a Malawi ngati unduna wake walephera kuteteza anthu pa za vutoli. CDEDI yati ndi zodabwitsa kuti sugar akusowa pa nthawi yomwe amayenera kupezeka kwambiri komanso kuti zomwe kampani ya Illovo yanena kuti anthu akuzembetsa sugar ndinkhani yodandaulitsa ndipo zikungosonyeza kuti pali zambiri zimene zikuzembetsedwa mdziko muno zomwe anthu sakudziwa. Namiwa wadzudzulanso kampani yaboma ya Salima Sugar ponena kuti "Sugar wake imangotchuka pamasamba amchezo koma sapezeka bwinobwino pa msika." #cfmnews #malawi
👍 😢 ❤️ 😮 😂 20

Comments