Capital FM Malawi
Capital FM Malawi
June 9, 2025 at 11:21 AM
Rhoda Gadama Misomali yemwe akufuna kuzapikisana nawo pa mpando wa phungu mdera la pakati m'boma la Mulanje lero aziwonetsera kwa akuluakulu ndi anthu ena a derali ngati phungu oyima yekha. Mwambowu ukuchitikira pa mudzi wa Nkhonya mdera la mfumu yayikulu Chikumbu m'bomali. Anthu osiyanasiyana asonkhana pa malopa kuti azalandire Gadama komanso kuzamva mfundo zake. Gadama Misomali anachita ganizo loyima pa yekha, chipani cha Democratic Progressive -DPP chitalengeza kuti zisankho za chipulula zomwe iye anapikisana nawo, anapambana ndi Damson Chelewani. #cfmnews #malawi
❤️ 👍 😂 🙏 4

Comments